Tsogolo la America Ndi Maiko Ena Aku Madzulo

Ulosi wa Baibulo umalosera za mtsogolo nthawi imene kudzakhala kopanda nkhondo, kumva chisoni ndi kulira. Mukawona zowawa, mikangano ndi mazuzo pa dziko pano simudabwa kuti chifukwa chiyani mulungu sakuthetsa mavuto amenewa panopa?

Ulosi wa Baibulo umatiwonetsa kuti mulungu ali ndi dongosolo, ndipo dongosolo lake lili lokhazikika. Anthu ambiri sadziwa dongosolo la mulungu kuti lili motani. Koma Baibulo likuwulula kuti dongosolo la mulungu ndi la nzeru ndi lodabwitsa kuyelekeza ndi mmene ife tingaganizira (Aroma 11:33; 1 Akorinto 2:9).

Zoona zake nzakuti, Baibulo limati dongosolo la mulungu likuyenera kugawidwa kwa wina aliyense (Chivumbulutso 21:7). Inde zonse zikuyenera kuti zigawidwe osasiyako kalikonse (Aheberi 2:8).

Mulungu akutinso dongosolo lake mlakuti akupange iweyo kukhala ngati iye mulungu (1 Yohane 3:1-2). Iye adzakupatsani ulemelero umene ali nawo (Afilipi 3:21) iye adzakupatsaniso mphamvu zochuluka komanso moyo wosatha (1 Akorinto 15:42-44, 53). Werengani ndie zimenezi kuti muwone zimene zikukambidwa. Izi ndi malonjezano odabwitsa.

Mulungu sangakanike kutipatsa zonse kuphatikizapo mphamvu zake komanso moyo wosatha pokha pokha akukhulupilire iweyo nthawi zonse kuchita zabwino ndi zoyenera. Njira yokhayo yomwe mulungu angakukhulupilire ndiyoti iweyo ukhulupilire mulungu basi.

Mulungu amadziwa kuti ukamukhulupilira udatha kuchita chilichonse. Udzatha kuchita zithu motsogozedwa ndi mulungu osati mwa iwe wekha ayi. Koma ngati sukhulupilira mulungu ndipo umawona ngati mulungu ndi wolakwitsa kapena kuti umadziwa zithu kuposa mulungu choncho mulungu sangakukhulupilire ndi mphamvu zake. Ukhoza kumachita zithu mwa iwe wekha osati motsogozedwa ndi mulungu zomwe zikhoza kubweretsa zowawa pa moyo wako wonse.

Cholinga cha mulungu ndi choti aphunzitse wina aliyense kuti akhulupilire mulungu kuti tisakhe kukhala mwa iye. Iyi ndi njira yokhayo yomwe ingatithandize kukhala ndi moyo wamuyaya ndi mwa mtendere.

Mudayamba mwalingalirako kuti chifukwa chiyani Mulungu watipatsa moyo wongoyembekezera pa dziko pano? Bwanji sanangotidutsitsa magawo onse a zowawa izi ndikutifikitsa ku moyo wosatha kuchokera poyamba.

Yankho lake mlakuti chifukwa choti pakufunika kukhala ndi kukhulupilira mulungu asanatipatse zonse zofunika.

Anthu ambiri amaweruza ndi kudzudzula mulungu chifukwa choti amalola zoipa ndi zowawa pa moyo wathu mdzikoli pomwe ali ndi mphamvu yothetsa zonsezi. Mulungu ndi wanzeru kuposa ife.

Kodi mulungu akhoza kuletsa zowawazi? Eya akhoza kuthetsa zowawa zonse. Koma kodi anthu angakhulupilire kumukhulupilira mulungu? Ayi, tikhoza kumaganiza kuti ndi zithu zosavuta. Njira yokhayo yomwe mulungu angatsimikize kuti ifeyo sitidziwa zonse ndiyo kuti aliyense ayesedwe.

Tsono kwa zaka zopitilira 6000 zapitazo, Mulungu wakhala akutilora kuti tiyende njira yanthu. Uwu ndiwo muyeso waukulu womwe mulungu anachita. Mulungu wapeleka mwayi kwa anthu ake kuti asakhe okha njira yomwe ili yabwino.

Kodi zikuyenda bwanji? Tili pa chiopsezo choti tikudziwononga tokha ndi nkhondo ya nyukuliya. Koma ngati mulungu salowererapo ndiye kuti tiwonongana tonse (Mateyo 24:22).

Zaka zikubwerazi zidzakhala zosautsa kwambiri, mulungu adzatilora kuti tiyambe kuwonongana tokha tokha iye asanabwere kudzatipulumutsa. Pamapeto pake munthu adzatsimikiza kuti munthu alibe mphamvu. Pomaliza munthu adzadziwa kuti mulungu ndiye ali ndi mphamvu komanso adzakhulupilira mulungu. Kenako adzadzayamba kukhulupilira mulungu komanso mulungu ndiye njira ya chooadi, moyo ndi mtendere.

Mulungu ali okozeka kutilora kuti tiyende njira yathu panopa ndikupeza mavuto ndikuphunzira kukhulupilira mulungu kuti atipatse moyo wosatha. “Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha iye amene analora kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana amulungu” (Aroma 8:20-21).

Njira yabwino

Inu ndi ine sitikuyenera kuphunzira kukhulupilira mulungu movuta ayi. Mulungu watipatsa kale chitsanzo cha njira yabwino. Tikupeza chitsanzo mu umoyo wa Abrahamu.

Dziwani zomwe mulungu anawuza Abrahamu mu Genesesi 12:1-3:

Tsopano Mulungu adati kwa Abrahamu, “Siya dziko lako ndi abale ako ndi nyumba ya bamboo wako ndipo upite ku dziko lomwe ndidzakuwonetsa. Ndipo ndzidzkupanga kukhala mtundu waukulu ndipo ndidzakudalitsa ndi kupanga dzina lako kukhala lotchuka ndipo udzakhala mdalitso. Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe ndi kutemberera onse okutemberera. Mitundu yonse padziko lonse lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

Amenewa ndi malonjezano odabwitsa. Mulungu analonjeza mtundu wa Abrahamu kuti udzakhala mtundu wotchuka kwambiri, ndipo mitundu ina idzadalitsika kudzera mwa iwo ngati angavomere zomwe mulungu wanena.

Kodi Abrahamu adati chiyani? Abrahamu adapita monga mmene mulungu ananenera (Vesi 4).

Abrahamu anakhulupilira mulungu, ndipo anavomera zomwe mulungu ananena kuti achite.

Izi ndi zomwe mulungu amafuna kuti inu ndi ine muchite povomera malonjezano. Iye akufuna kuti tikhale ndi chikhulupiliro chenicheni – ndi kuchita zomwe mulungu anena kuti tichite bwino.

Chifukwa Abrahamu anakhulupilira ndi kumvera, Mulungu anapitiliza kupeleka malonjezano kuchokera kwa Mulungu.

Dziwani kuti malonjezano onse amene mulungu analonjeza Abrahamu mu Genesisi 17:1-8.

Tsopano pamene Abramu anali ndi zaka 99, Mulungu anawonekera kwa Abramu ndipo anati, “ndine mulungu wamphamvu. Ndimalhala nawo ndipo siiwe ochimwa. Ndipo ndidzapanga pangano la pakati pa iwe ndi ine ndipo ndidzachulukitsa mtundu wako.

Abramu anagwetsa khope yake pansi ndipo mulungu adati, “kwa ine pangano ndi iwe udzakhala tate wa fuko lonse ndipo dzina lako silidzatchedwanso Abramu kutathauza kuti tate wokwezedwa koma udzakhala Abrahamu kutathauza kuti tate wa fuko. Dzidzakupanga kukhala wachuma chochuluka ndipo ndidzapanga mafuko ena kuchokera kwa iwe. Ndidzakhazikitsa pangano pakati pa ine ndi iwe komanso mtundu wako komaso m’badwo ukubwerawo. Dzidzakupatsa dziko la malonjezano la Kanani lomwe mudzakhala mpaka muyaya.

Abrahamu adakhulupilira zomwe mulungu adanena.

Patapita zaka zochuluka, mulungu anayesa chikhulupiliro cha Abrahamu pomuuza kuti apelike msembe mmwana wake Isake (Genesisi 22). Awa anali mayesero a chikhulupiliro.

Kodi mukadatani?

Abrahamu sanadziwe chifukwa chimene anawuzidwira kuti apelike msembe mwana wake. Komai ye sanawilingule. Sanafune kuti mulungu afotokoze zifukwa zochitira izi. Sanafune kukana za pemphero.

Abrahamu anakhulupilira mulungu. Iye anakhulupilira kuti mulungu sanama. Iye anakhulupilira kuti mulungu anali ndi zifukwa zokwanila popeleka lamulo limeneri. Iye anakhulupilira kuti akamvera mulungu adzapulumutsira mwana wake Isake chifukwa mulungu anamulonjeza kuti adalitsa mtundu wake kudzera mwa Isake (Aheberi 11:17-19).

Ndiye Abrahamu anamvomera. Iye anakhulupilira mulungu kwambiri. Ndiye chinachitika ndi chiyani? Mulungu anamuletsa Abrahamu kuti apeleke msembe mwana wake Isaki motero anatumiza nkhosa kuti Abrahamu apelike msembe mmalo mwa mwana wake Isaki.

Tsopano poti Abrahamu anawonetsa kukhulupilika kwa mulungu powonetsa kukhulupilika mulungu anapeleka malonjezano ake kwa Abrahamu.

Ndipo anati, ndikulumbira mwa ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi,wosandikaniza mwana wako yekhayo, ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengamlenga komanso ngati mchenga wa mphepete mwa Nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda zidzalanda mizinda ya adani awo, ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi lidzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.” (Genesisi 22:16-18)

Malonjezano amenewa sanali kwa Abrahamu kokha ayi komanso kwa ana a Abrahamu. Ndipo malonjezo anali magulu awiri. Monga mukudziwa Abrahamu anali ndi ana magulu awiri.

  1. Ana ake a Abrahamu eni eni a magazi

  2. Ana a Abrahamu a mu uzimu – Kapena kuti omwe amatsatira ndi kumvera chikhulupiliro cha Mulungu (Agalatiya 3:26-29).

Abrahamu ndi tate wa ma fuko onse komanso tate wa ana ochuluka mwa njira zambiri. Inde pali mafuko ochuluka amene ali ana eni eni a Abrahamu amene analandira madalitso kuchokera kwa Abrahamu. Abrahamu adzakhala tate wa mafuko onse komanso mafuko onse adzadalitsika kudzera mwa iye.

Ana eni eni a Abrahamu

Tsopano tiyeni tiwone zomwe Baibulo limanena za ana eni eni a Abrahamu mmasiku omaliza.

Dziwani kuti malonjezano amene mulungu adapanga ndi Abrahamu anadutsa kwa mwana wake Isake (Genesisi 26:1-5; Genesisi 28:13-14).

Mulungu anawulura zonse za mtsogolo la Yakobo amene analembedwa mu m’buku la Genesisi monga:

  • Mfuko la Yakobo lidzachuluka kwambiri ndipo lidzadzadza dziko lonse (Genesisi 28:13-14)
  • Mu Genesisi 49, Yakobo ananeneratu za zomwe zidzachitike kwa ana ake onse payekha payekha mmasiku otsiliza. Apa akuwulura kuti Yosefe adzadalitsika kwambiri kupambana wina aliyense mwa ana ake.
  • Mu Genesisis 48, Yakobo ananeneratu za mtsogolo la ana a Yosefe amene ndi Eferemu ndi Manase.

Genesisi 48 ikukamba za nkhani ya Yakobo mmene anatengera ana awiri. Mwa njira iyi Yosefe analandira magulu awiri a chuma kuchokera kwa makolo ake.

Pamen Yakobo anadalitsa Eferemu ndi Manase, anasanjika dzanja la manja pa Eferemu amene anali wang’ono. Yosefe anaganiza kuti poti bamboo wake anali wa khungu analakwitsa.

Ndipo anati kwa kwa bambo wake sichoncho bambo wanga chifukwa uyu ndi mwana woyamba musanjike manja pa mutu pake. “Koma bamboo wake anakana ndipo anati ndikudziwa mwana wanga. Iyeso adzakhala anthu anga komanso adzachita bwino. M’bale wake wang’ono adzakhala wopambana komanso mtundu wake udzakhala wamphamvu.”

Apa Yakobo analosera kuti Maqnase adzakhala mtundu waukulu koma m’bale wake Eferemu adzakhala mtundu wamphamvu.

Kodi izi zidzachitika liti?

Mu phunziro loyamba munaphunzira kuti za zaka 2520 zaka za chilango kwa ana a Israelezomwe zinayamba pamene a Israele anachoka pamanso pa mulungu kumapeto kwa ulamuliro wa mfumu Solomoni. Zaka za chilangozi zidatha mu chaka cha 1585. Iyi ndi nthawi yomwe maiko a ku ulaya monga Nertherlands, France, England, Denmark, Norway, Iceland, Ndi Sweden anayamba kutukuka pa chuma ndi mphamvu. Poti maiko amenewa anakwanilitsa ulosi wa ana a Israele ndipo tikhoza kunena kuti maiko amenewa akuyimira ma fuko khumi a ana a Israele.

Israele inalinso ndi nthawi ya chilango ya chiwiri yomwe inayamba pamene ma Asiliya anayamba kutenga ana a Israele kupita nawo ku ukapolo ku dziko lawo mu zaka za 733 BC. Choncho chaka cha 2520 chidatha mu chaka cha 1788.

Pa nthawi imeneyi dziko la United Kingdom inayamba kulowa mmalo mwa dziko la France ngati dziko la mphamvu kwambiri pa dziko lonse lapansi. Dziko la Austraria linakhazikitsidwa mu chaka cha 1788. Dziko la Britain linapitilira kukula mpaka liakwanitsa kulamulira mbali ina ya dziko.

M’bale wake wa Eferemu, Manase ndiye anali ngati dziko la Amerika. Maiko onse amene anali pansi pa Briatin aku Amerika analandira ufulu wodzilamulira kuchokera ku Britian mu chaka cha 1776. Patadutsa izi maiko onse adapepha kuti maiko onse apange mgwilizano omwe umadziwika kuti United Nation ( Gwilizano wa maiko onse). Ndipo izi zidachitika mu chaka cha 1788 pa 21 Juni pomwe padayambira mgwilizano wa maiko aku Amerika. Chonco Amerika lidakhala dziko lolemera kwambiri komanso lamphamvu kukwanilitsa ulosi wa mu Genesisi kuti Manase adzakhala wamphamvu.

Mdalitso sunabwere kwa a Israele osati chifukwa choti anali abwino kuposa onse ayi. Baibulo limati kwa a Israele, ”Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulutenge popeza ndiwe wokanika,” (Deuteronomo 9:6) dziwa kuti izi zabwera chifukwa choti Abrahamu anakhulupilira mulungu ndi kusunga mawu ake ndi malamulo ake (Genesisi 26:5).

Koma ndi kubwera kwa madalitso amenewa kwabweranso ndi udindo omvera mulungu. Mulungu anasakha Israele ngati dziko lachitsanzo. Ngati amvere mulungu adzakhala a chitsanzo chabwino kwa ena kuti amvere (Exodo 19:5), Deutoronomo 4:5-8,) Koma ngati akane mulungu ndi malamulo ake mulungu adzawalanga anthu onse (Aroma 2:9).

Kodi Israele anamvera mulungu? Kodi maiko onse aku ulaya ndi anthu owopa mulungu?

Koma ayi, zoona zake nzakuti Israele walero ali patsogolo kukana mulungu.

Mu Levitiko 26 ndi Deuteronomo 28, Mulungu akuwulura za zimene adzachitire dziko la Israele ngati apitiliza kukana mulungu. Ma ulosi amenewa anakwanilitsidwa kale kale koma kukwanilitsidwa komaliza ndi nthawi ya panopa. Ndipo zonsezi zikukwanilitsidwa lwero lino.

Tiyeni tiwone zilango zomwe mulungu analnena mu Levitiko 26, maka kuyambira mu vesi 14.

  1. “Kudzakhala nkhondo ndi mikangano.”

    Ziwembu zomwe zinachitika ku dziko la Amerika pa 11 September 2011 inali chabe imodzi mwa nkhondo zomwe ana a Israele ndi Yuda amayenera kukumana nazo. Kuwomberana ndi ziwembu zachuluka dziko la Amerika komanso maiko a Israele.

  2. “Matenda ndi mlili zomwe zidzawononga anthu.”

    Izi zikuwoneka pa matenda ochuluka amene alipo monga Edzi amene akhala akusowetsa mtendere pa dziko lapansi. Kodi matenda amenewa simudziwa kuti akufala chifukwa chosamvera mulungu? Zotsatira zosamvera malamulo a mulungu monga chigololo ndi zina mwa zomwe zikuyambitsa matenda amenewa.

  3. “Mudzalima mbewu koma sumudzakolola.”

    Ndi maiko ati omwe amatumiza zakudya ku maiko ambiri mu dzikoli?Amagula ndi ndani?Wonani nokha.

  4. “Mudzagojetsedwa ndi adani anu.”

    Zidachitika ndi chiyani ku Afuganstan?

  5. “Amene mumadana nawo ndi omwe adzakulamulireni.”

    Tawonani makhalidwe a atsogoleri amaiko anu, omwe sakhala ndi chidwi chosamala anthu awo.

  6. “Mudzathawa popanda okuthamangitsani.”

    Chifukwa chiyani Asilikali a dziko la Amerika anathawa ku Afganistan popanda owathamangitsa.

  7. “Ndidzakuchotserani mphamvu chifukwa cha kunyada kwanu.”

    Alipo mdzikoli omwe ali ndi kuthekera kuthetsa mikangano yomwe ilipo pakati pa Amerika ndi Afganistan? Kodi Russia, china, North Korea ndi ena amakhulupilira za mphamvu ya Amerika kuti ndiyochepa kuti akhoza kuchepetsa mphamvu zake?

  8. “Ndidzasitha nyengo zanu, kupangitsa nthaka kukhala yosabala zipatso.”

    Ganizirani njala ndi chilala chomwe chikupitilira mdziko la America ndi Australia.

Matemberero ayamba kale kuwoneka panopa. Ichi ndi chiyambi cha chilango cha mulungu.

Ma ulosi akupitilira kunenera zithu zomwe zidzawoneke, panopa pamene ndikulemba phunzilori. Izi ndi zomwe zikuwoneka mu nthawi ya Israele ndi Yuda watsopano (Levitiko 26:23-39).

  • Zilombo zoopsa zidzafika mmisewu mkupha anthu
  • Nkhondo dziko lonse
  • Matenda ndi mlili paliponse
  • Kugonjetsedwa ndi adani
  • Njala
  • Anthu adzadyani okha okha nthawi ya njala.
  • Mizinda idzawonongedwa
  • Anthu adzatengedwa ukapolo

Ndi zovuta kukhulupilira. Koma ndi zomwe zidzachitike kwa Israele ndi Yuda kale. Ndipo zidzachitikanso mtsogolo – pokha pokha maiko amenewa abwererenso kwa mulungu.

Ulosi ukuti maiko amphamvu adzagojetsedwa ndipo sadzakhalaponso. Israele ndi Juda adabalalika pakati pa maiko ena, adzagulitsidwa ngati akapolo ndipo zoopsa zazikulu zikubwera zopesera apa.

Ulosi umenewu sikuti wanenedwa kamodzi ayi. Koma ukubwerezedwa bwerezedwa nthawi ndi nthawi mu Baibulo.

Tawonani buku la Ezekiele. Ezekiele anali mneneri pakati pa Ayuda anatengedwa ukapolo ku Babeloni. Koma uthenga wa Ezekiele sunali wa Yuda okha. Mulungu anatumiza Ezekiele ku Israele, ” ndikukutuma kwa ana anga ku Israele, ku dziko lowukira mulungu lomwe lachimwira ine (Ezekiele 2:3).

Ezekiele anapeleka unthenga wochenjeza, kuwauza za kutengedwa ukapolo ngati Israele salapa machimo. Koma Israele anali atapita kale ku Ukapolo kwa zaka 125. Uneneri wake sunali wa nthawi imeeneyo koma panopa.

Werengani Ezekiele 5. Ikupeleka unthenga wa mmene Israele adzagonjetsedwere. Komanso kuti ndi angati adzafe nthawi imeneyo.

“Ambiri mwa iwo adzafa ndi lili, adzazuzika ndi njala. Ena adzafa ndi nkhondo” (Ezekiele 5:12).

Ambiri mwa anthu a Israele lero lino adzafa pa nkhondo ndi njala. Ndipo otsalawo adzatengedwa mu ukapolo.

Dziwani za Deuteronomo 28:68, “Mulungu adzakutulutsaninso ku Aeguputo ndi ngalawa. … ndipo adzakugulitsani kwa adani anu nonse akazi ndi amuna omwe ndipo palibe amene adzakugulani”. Izi sizinachitike mu mbiri ya dziko. KOma ndi uneneri womwe ukubwera mtsogolo muno.

Mneneri Mose ananena kuti, “zoipa zidzakupezani mmasiku omaliza, chifukwa mwachita choipa pa maso pa mulungu, mwamuyamba dala mulungu chifukwa cha zochita zanu” (Deuteronomo 31:29).

Yesaya, Jeremia, Hoseya ndi aneneri ena ananena za kugojetsedwa kwa Israele ndi Yuda. Uneneri ndi wa zoona ndipo ulosi umenewu udzachitika ndithu.

Nkhani yabwino ndi yakuti masiku amavuto akubwezeretsa Israele kubwerera kwa mulungu ngati tikhulupilira mulungu. Nkhani iyi ndi ya tsiku lina.

Kodi mwaphunzirapo chani mu phunziro la ulele limeneri? Chonde pezani ka nthawi kufunsa anthu ena kuti alowe nawo mgulu ili lophunzira mawu a Mulungu.

Gawani unthengawu pa masamba onse a mchezo.