Zomwe German Ikuchita Zokhudza Masiku Otsiliza

Nkhondo ya pakati pa Russia ndi Ukraine ya mchaka cha 2022 yadabwitsa dziko lonse la pansi.

Zomwe Putin wanena zoopseza kuti agwilitsa ntchito ma bomba a nyukiliya zabweretsa mantha pakati pa anthu kuti mwina zikhoza kuyambitsa nkhondo ya dziko lonse la pansi ya chitatu (World War 3). Patatha masiku ochepa nduna yaikulu la dziko la German walonjeza kuti agwilitsa ntchito ndalama zambiri zokwana 100 biliyoni dola kuti akozeso ntchito za nkhondo. Mayiko ambiri ayamba kale kufuna kukhala nawo m’magulu ndi maubale a padziko lapansi monga European Union (EU) komanso NATO.

Kodi zonsezi zithera kuti? Kapena kuti zikupita kuti.

Kodi Baibulo limati chiyani za ulosi wa tsogolo la maiko a ku Europe, Russia ndi maiko ena onse a dziko lapansi.

Babeloni wagwa

Buku la Chivumbulutso linayakhula kale za mzinda waukulu wa “Babeloni” womwe ukulamulira ma mfumu onse a dziko lapansi m’masiku omaliza (Chivumbulutso 17:5,18). Babeloni ameneyu akuimira zuthu zokhudzana ndi ndale, zachuma komanso mphamvu ya chipembedzo yomwe idzabwere kudzalamulira dziko yesu asanabwere kudzaweruza dziko lapansi (Chivumbulutso 18).

Kodi Babeloniyu ali kuti panopa?

Kodi ulamuliro wa ndale komanso mphamvu ya chipembedzo ikuwoneka pati mu zochitika za mdziko lerori?

Yankho lake lili mu Daniel 4.

Mu unthenga wa mneneri umenewu ukusonyeza kuti Babeloniyi alipo kale.

Kumapeto kwa phunziro ili, chonde mupeze nthawi kuti muwerenge Daniel 4. Panopa tiyeni tiwone mwachidule nkhani yonse.

Nebukadineza, mfumu yaku Babulo analota maloto omwe amawonetsa mtengo waukulu ndi wautali womwe umapeleka mnthunzi komanso umapeleka chakudya kwa mbalame zonse ndi nyama zonse pa dziko lapansi. Kenako mtengo uja unadulidwa ndipo m’bali mwake adaikamo ma unyolo achitsulo kwa nthawi yaitali.

Ndipo mfumu idawona woyerayo akutsika kuchokera ku mwamba akuti “dulani mtengowu, muwuwononge, komanso musiye chiphukira pansi ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi maunyolo ndi zitsulo za mkuwa, ndipo mulisiye kuthengo pakati pa udzu. Anyowe ndi mame mpaka papite zaka zisanu ndi ziwiri.

Tanthauzo lake.

Inu mfumu kumasulira kwake ndi uku: zimenezi ndizo zimene mulungu wamphavu zonse watsimikiza kutitu zidzakugwereni. Mudzachotsedwa pakati pa anthu. Mudzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo. Mudzadya udzu ngati ng’ombe, ndipo mudzanyowa ndi mame zaka zisanu ndi ziwiri. Apo mudzavomereza kuti Mulungu wopambana zonse amalamulira ma ufumu onse a anthu, ndipo kuti angathe kulonga munthu aliyense monga afunira. (Daniel 4:23-26)

Patatha chaka chimodzi uneneri uja udakwanilitsidwa. Mulungu anachotsa nzeru ndi mphamvu za Nebukandineza ngati chilango chifukwa cha kunyada kwake. Kenako patatha zaka zisanu ndi ziwiri, Nebukandineza nzeru zake zidabwereranso ndipo adabwereranso kukhala mfumu kulamulira mzinda wonse wa Babeloni.

Chifukwa chiyani ulosi umenewu ukupezeka mu Baibulo?

Dziwani kuti Daniel sanalembe ulosi umenewu mpaka utakwanilitsidwa. Choncho ulosi uwu sukutiuza chilichonse cha mtsogolo pokhapokha ngati ngati waloseledwanso kachiwiri. Ndipo ndi zoonadi kuti unakwanilitsidwa kachiwiri.

Monga Babeloni anakhala opanda mfumu kwa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anachita misala ndipo tikhoza kufunsa kuti kodi “nthawi ndi chani?”

Mu Baibulo nthawi ndi nyengo ya masiku 360. Tadziwa bwanji za izi? Tikawerenga Chivumbulutso 11:2-3 ikukamba nthawi yomwe yafotokozeredwa ngati “miyezi 42” komanso masiku “1260”. Mu Chivumbulutso 12:14 nthawi yomweyo ikutchedwa “nthawi” pomwe akuti mayi uja adasungidwa zaka zitatu ndi theka. Choncho tikhoza kutsimikiza kuti nthawi ndi masiku 360.

Kuti timvetsetse kukwanilitsidwa kwa chiwiri kwa Daniel 4, tikuyenera kudziwa kuti ma ulosi a Baibulo tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi. Werengani Numeri 14:34 and Ezekiele 4:6 kuti mutsimikize za izi.

Mu kukwanilitsidwa koyamba kwa Daniel 4, Babeloni adali opanda mtsogoleri kwa masiku okwana 2520 (7x360=2520) zomwe ndi zaka zisanu ndi ziwiri.

Mu kukwanilitsidwa ka chiwiri kwa ulosi wa Daniel, Babeloni anali opanda mtsogoleri kwa zaka 2520 zomwe zili zaka zisanu ndi ziwiri. Mulungu anagwetsa Babeloni ndi ufumu wake ndi kuika maunyolo a zitsulo m’mbali mwake kuteteza kuti ungakule kwa zaka 2520. Koma kumapeto kwake Mulungu anachotsa maunyolo aja, panthawi imeneyi mtsogoleri watsopano adabwera kudzalamulira. Mtsogoleri ameneyu ndiye amene adafotokozeredwa mu buku la chivumbulutso ndipo adayamba kukulanso.

Babulo ameneyu akukulabe mpaka pano ndipo tonse tikuona ndipo apitilirabe kukula mpaka akwanire dziko lonse lapansi.

Kodi zidachitika liti?

Monga tikudziwa kuti patadutsa maloto a Nebukandineza mu Daniele 4, ndime yotsatira yake inadupha mkufotokoza za kugwa kwa Babulo. (Monga mabuku onse aneneri mu Baibulo buku la Daniele laikidwa mu mitu ikulu ikulu osati kufotokoza nkhani yonse mwatsatanetsatane.

Pamene mfumu ya Babulo anali kudya pa phwando, dzanja linawoneka likulemba khoma. Mfumu idaitana Daniele kuti awerenge ndi kutanthauzira mawuwo omwe adalembedwa pa khomawo. Ndipo Daniel adafotokozera kuti mawuwo akutanthauza kuti ufumu wa Babulo watha ndipo Mulungu wapeleka kale ufumuwo kwa wina amene ndi Amedi ndi Apesi.

Zoonadi Amedi ndi Apesi atenga kale ufumuwo ndipo agonjetsa kale, ndipo alanda mzinda usiku wa lero. Tikhoza kufufuza za tsiku lenileni lomwe izi zidachitikira poti ena amati zidachitika pa tsiku la khumi ndi chinayi mwezi wa Babeloni.

Mzindawu udagwetsedwa pa tsiku la khumi nchinayi mwezi wa Babeloni. Ndipo patadutsa masiku awiri, Daniele adauza mfumu kuti Babulo wapelekedwa kwa Amedi ndi Apesi ndi pa usiku omwewo Babulo agwa.

Tathauzo la mawu omwe adalembedwa pa khoma ndi motere:

  • Mene – Ndiye kuti Mulungu wawerenga masiku a mfumu wanu ndipo awuthetsa.
  • Tekele - Ndiye kuti mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapelewera.
  • Para sini - Ndiye kuti ufumu wanu wagawidwa kwa Amedi ndi Apesi

Kodi Germany idzalamulira dziko lapansi?

Daniele 4 akukwanilitsidwa pomwe tikuwona Germany yatenga mphamvu, izi zinachitika pa 1 October 1982 pansi pa utsogoleri yemwe dzina lake ndi Helmut Kohl. Zoti Germany ikhala ndi mphamvu zolamulira dziko lonse tikhoza kuona zithu izi.

  • Patangotha zaka 8 pansi pa ulamuliro wa Helmut Kohl mbali ya kummawa ndi kumadzulo dziko la Germany idagwilizana zokhala mu ulamuliro umodzi- zomwe zidachitika tsiku lofanana ndi kugwetsedwa kwa Babulo pa 3 October 1990.
  • Kohl adayetsetsa kukhazikitsa ma ubale pakati pa maiko ena ku Europe komanso adabweretsa ganizo logwilitsa ntchito ndalama imodzi m’maiko onse aku Europe ndiso kuyambitsa mgwilizano wa maiko onse a ku Europe monga EU (European Union).
  • Kohl ndi atsogoleri ena adapangitsa Germany kukhala dziko lotchuka ku Europe komanso kupanga Europe kukhala yotchuka dziko lonse lapansi.

Mwayi omwe ulipo pa nkhani zonsezi ndi wakuti zonsezi zikuchitika mofanana ndi momwe adaloseledwera zaka 2500 zapitazo.

Kumbukirani kuti Daniele 4 akufotokoza za maunyolo a zitsulo pa phukira za mtengo omwe udadulidwa, mmene udachotsedwa pa 1 October 1982. Izizi zikuwonetsa kuti pali utsogoleri watsopano, Babeloni watsopano wayamba kumera kapena kuti kuphukira mizu kuonetsa kuti Babulo watsopano wabwera.

Ma ulosi onse a Baibulo amachokera kwa Mulungu ndipo Mulunguyo akanena zimachitika monga mowe walozera pa nthawi yake.

Kodi ndi ndani akhale ndi mphamvu mu 21 Century?

Europe watsogozedwa ndi German, komanso mabungwe onse a zachipembedzo adzakwanilitsa ma ulosi onse a Baibulo okhudza masiku omaliza.

Mu ulosi wa Baibulo ukuwonetsa kuti Babeloni uyu adzalamulira dziko lonse lapansi kuphatikizapo Russia, China ndi maiko ena.

Mu maphuniro ena mtsogolomu muphunzira zambiri za ufumu umenewu komanso mafumu khumi amene adzatengepo gawo pa kutha kwa dziko. Padakali pano wonetsetsani mmene Babulo- Germany ndi Europe agwilizanitsire mabungwe a chipembedzo poyankha za chiopsezo cha Russia.

Phunziro lotsatira likupatsirani zosowa zonse za momwe mungamasulire ma ulosi a aneneri.

Osaiwala kuwerenga Daniel 4 yense kuti muvetsetse za zomwe mwaphunzira.

Chonde gawani unthengawu kwa anzanu m’masamba onse a mchezo.